Amakufunirani moyo wathanzi – Mtumwi Joseph Ziba

Amakufunirani moyo wathanzi - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 25 February, 2019

Amakufunirani moyo wathanzi – Mtumwi Joseph Ziba

Itafika nthawi ya madzulo, anabweretsa kwa iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda, ndipo iye anatulutsa ziwandazo ndi mawu ake, nachiritsa odwala onse. Kuti zikwaniritsidwe zimene ananena mneneri Yesaya kuti “Iye anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu”. Mateyu 8:16-17

Chifukwa cha kusadziwa malemba ndi kusamvetsetsa chikondi cha Mulungu, pali anthu ena amene amanena kuti nthenda, zipsinjo komanso mazunzo zimachokera kwa Mulungu. Mumawamva akuti “Mulungu wandipatsa nthenda iyi ndi chipsinjo ichi kuti andiphunzitse china chake kapena kundilanga”.
Komano, Mulungu woyera chonchi angapange bwanji chinthu choipa chonchi kwa anthu? Baibulo limati “Chomwecho, ngati inu (anthu), muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa inu?” (Mateyu 7:11).
Ndikholo lotani limene mwana wake akamavutitsa amaitana dotolo nati “Chotsani khutu limodzi kapena mwendo umodzi kuti mwanayu alangike, poti ali ndi mwano?” Simungapange zoterozo ayi! Tsono muyembekezera bwanji Mulungu amene amatchedwa chikondi kuti angakupatseni nthenda ndi zipsinjo pofuna kukulangani? Sangatero ayi.

Chifukwa china chimene Yesu Khristu anabwelera kudziko lino (pambali pozathana ndi tchimo) chinali kudzatenga zipsinjo ndi nthenda zathu. Izi ndi zomwe lemba tawerenga pamwambapo likutitsimikizira.

Makamaka likutsindika kunena kuti “…ndipo Iye anaturutsa ziwandazo ndi mau ake, NACHIRITSA ONSE OMWE ANALI ODWALA…” Mwachigwira chimenecho? Ngati Yesu anachiritsa aliyense yemwe anali odwala, mudzindikire kuti ndichifuniro cha Mulungu kuti inu musamadwale. Amafuna mukhale moyo wathanzi!!.

Baibulo manenanso kuti, “za Yesu waku Nazarete, kuti Mulungu anamzodza Iye ndi mzimu oyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachitachita zabwino, NACHIRITSA ONSE OSAUTSIDWA NDI MDYEREKERI, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye” (Machitidwe 10:38)

Mulungu anamzodza Yesu ndipo anakhala naye ndicholinga choononga nthenda ndi zipsinjo. Mwaichi mukadwala osalola mdani kukunamizani kuti ndi chilango chochoka kwa Mulungu, koma kanani mu dzina la Yesu.

CHIVOMEREZO
Atate wabwino, zikomo polankhula malingaliro anu kwaine. Mumandifunira moyo wathanzi. Sindingadwale pakuti ichi ndicho chifuniro chanu Mzimu oyera amakhala mwaine- moyo uli mwa ine uli ndi mphamvu yokutha kugonjetsa matenda. Palibe nthenda zomwe zingakhale mu thupi langa. Mu dzina la Yesu.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *