Atsendera Chaka ndi Ubwino Wake – M’tumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 10 Disembala 2018
Atsendera Chaka ndi Ubwino Wake – M`TUMWI JOSEPH ZIBA
Mubveka chakaci ndi ukoma wanu; Ndipo mabande anu akukha zakucha. Masalimo 65:11
Mulungu amakhala kwa muyaya koma anatiika padziko lapansi pamene pali nthawi, ndipo amalemekeza nthawi. Baibulo ku Mlaliki 3:1 limati; Kanthu kali konse kali ndi nthawi yache ndi chofuna chiri chonse cha pansi pa thambo chiri ndi mphindi yache.
Chaka chino sichikuyenera kumalizika popanda inu kulandira za ubwino wake. Lemba liri m’wambali likutitsimikizira kuti Atate amatsendera chaka ndi ubwino wake.
Mathero a chaka malingana ndi Mulungu ndi nthawi yokolora, m’chifukwa chake mukuyenera kuona kuchulukitsidwa kwa Mulungu mu mwezi umenewu.
Nkutheka simunaone ndi kukhudzapo ubwino wake, mu utumiki, m’banja, ntchito, malonda, maphunziro ndi zina zambiri. Lorani mwezi uno ukhale wanu. Mwafika munthawi imene muuzimu zokolora zanu zacha, kotero zikonzekeretseni potamanda ndi kuthokoza.
Malemba amati nthawi yokolora ndiyo nthawi yotamanda ndi kuthokoza. Musalore mdyerekezi kapena wina aliyense akukhumudwitseni. Kondwerani munthawi iliyonse yopezeka m’mwezi umenewu ndi mtima wodzala ndi matamando ndi mathokozo ndipo mudzakolola mochuluka za chisomo, kukonderedwa ndi zina zambiri.
CHIVOMEREZO
Atate, zikomo koposa kaamba kotsendera chakachi ndi ubwino wanu. M’chisomo chanu ndikutenga ndi kunenerera chikwaniritso cha uneneri wonse umene mau anu anayankhula kwa ine. Matamando ndi mathokozo zikhala ndi ine masiku onse m’mwezi uno poti ndiyo nthawi ya kholora langa. M’dzina la mphamvu zonse la Yesu, Amen.
#ApostleJosephZiba #FountainofVictory #InfallibleProofs #LifeUndenied
Recommended Posts

He Sympathises with Us – Monday, 18th January, 2021
January 18, 2021

Custodians of the Good News – Monday, 11th January, 2021
January 11, 2021