Chisankho n’chanu kukhala moyo wochita bwino – Apostle Joseph Ziba

Chisankho n’chanu kukhala moyo wochita bwino - Apostle Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 24 December, 2018

Chisankho n’chanu kukhala moyo wochita bwino Ndi M’tumwi Joseph Ziba

Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru. Yoswa 1: 8 KJV

Tsiku lina, posinkhasinkha ndi kullingalira Mawu a Mulungu, Atate adanditsegula maso ku mfundo zomwe zimapangitsa munthu kupambana mwaumulungu m’moyo uno. Pamene ndinkangokhalira kukondwera ndikudziviika mu zomwe Atate amavumbulutsa, Iye anandifusa funso lomwe limaoneka ngati “losamvetsetseka.’ Iye anati:

“Mwana wanga, Kodi umaganiza kuti n’chifukwa chiyani ndidayikiza mfundo zokhudzana ndi kuchita bwino kwa moyo mwa umulungu?” Ndinakhala chete mwakathawi ndikuganizira mozama zoti ndiyankhe. Kenako anapitiriza nati, “N’chifukwa chiyani mumayenera kutsatira mfundo monga kupereka chachikhumi, kubzala mbewu, kupereka zipatso zoyamba, kupatsa osauka ndi ena?”

Ndisanayankhe nkomwe, Iye anati; _”Ndakupatsani mfundo zonsezi kuti mulingirire choonadi chimodzi chofunikira; ichi ndiye choti kupindula ndi kuchita bwino m’moyo zimatengera chisankho cha munthu “.

Kenako adandifotokozera kuti kukhala osauka kapena olemera m’moyo uno, zimatengeranso chisankho cha munthu. Kotero, Iye amapereka mfundo zimenezo kuti munthu asankhe mtundu wa moyo womwe akufuna kukhala – kaya wosauka kapena wolemera (malingana ndi kuti wina amatsatira mfundozi kapena ayi).

Tsopano ndi moyo wotani umene mukufuna kukhala? Kodi mukufuna kukhala osangalala ndi wachuma? Kapena mukufuna kukhala wosawuka ndiozunzika? Zonse ziri kwa inu. Chinthu chabwino kwambiri chimene Mulungu anachita chinali kuyika mfundo zake m’Malemba; kotero mumasankha.

Zoti mudziwe; kupambana m’moyo sikukhala ndi ndalama zokha, ayi; kumathanso kuwonekera madera osiyanasiyana a moyo. Pa malemba opatulika, kupindula kumatanthauza kuyenda bwino kwa moyo wanu kapena kuti kukwaniritsa zomwe mumapanga popanda chovuta chilichonse. Inde, kupambana ndipamene inu mukuchita bwino m’mbali zonse za moyo wanu – zikhale mu thanzi lanu, moyo wa banja lanu, ndalama, ntchito, zamaphunziro ndi madera ena onse.

Sankhani kutsatila mfundo zake lero ndipo mudzapindula njira yanu.

PEMPHERO

Atate, mu Dzina Lamphamvu la Yesu, zikomo potsegula maso anga kupyolera mu Mawu anu. Malamulo anu onena za kuchita bwino kwanga m’moyo uno ngowonekeratu m’Malemba. Ndikudzipereka ndekha kuchiphunzitso cha mau anu ndikutsatira mfundo zanu kuti ndipindule nazo. Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *