Chitetezo cha Moyo wanu N’chotsimikiza – Mtumwi Joseph Ziba

Chitetezo cha Moyo wanu N’chotsimikiza - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 21 January 2019
Chitetezo cha Moyo wanu N’chotsimikiza – Mtumwi Joseph Ziba

”Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani kapena kukutayani konse.” Ahebri 13:5 CCL

Chimodzi mwa zinthu zimene Satana amachita ukamadutsa m’mafunde a moyo uno ndikukutsimikizira kuti uli wekha ndipo Mulungu sali nawe.

Komabe, khalani otsimikizika mwa mawu ake kuti Mulungu sadzakusiyani kapena kukutayani konse. Chomwecho m’nyengo yowawitsayo, onani Mulungu.

Bayibulo pa Masalimo 27:5, likukamba mwachimvekere:
“Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza m’malo ake okhalamo; adzandibisa m’kati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.”

Mulungu amakubisani nakutetezani m’nthawi ya mavuto moti Satana sangakukhudzeni. Kotero osalora nyengo iliyonse kukukanikitseni kuwona zimene Mulungu akupanga. Ndipo ingakhale m’mavuto momwemo, mwetulirani ndikunena, “Iye anati sadzandisiya ndipo sadzanditaya”.

Kulakwitsa kumene mungachite pamene muli m’mavuto, ndikukuza mavuto anuwo kuposera Mulungu. Mukatero, mumpatsa mpata oyipayo kuti akuwonongerenitu.

Koma, ndikufuna mumchititse Satana manyazi pamene iyeyo akuwona ngati inu muyiwala thandizo la Mulungu m’nthawi ya mavuto. Chitani zosiyana ndi zimene iye akuganiza; kondwerani ndi Mulungu amene amakhala nanu nthawi zonse, ndipo oyipayo adzakuchokerani.

PEMPHERO
Ndine otetezedwa, ndipo palibe nyengo imene ingandigonjetse. Ndikhala m’nthuzi wa Atate anga amene andibisa ine m’chihema, kotero Satana ndi amithenga ake sangandikhudze. Chitetezo changa ndichotsimikizika. M’dzina la Yesu, Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *