Dalirani Mawu Ake – Mtumwi Joseph Ziba

Dalirani Mawu Ake - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 27 May 2019
DALIRANI MAWU AKE – Mtumwi Joseph Ziba

“momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m’mene ndinawatumizira.” Yesaya 55:11 (Buku lopatulika)

Cholakwika chachikulu chimene mungapange ndi ku taya mtima ndi Mulungu, ndi kuganiza kuti mawu ake sangakusintheni.

Mutha kukhala kuti mukudutsa mu nyengo zowawitsa, ndipo zinthu sizikuyenda Mnyengo zina. Ngakhale zili choncho phunzirani kudalira mawu a Mulungu mu nyengo ngati zimenezi.

Vesi lili pamwambalo likuti mawu a Mulungu adzachita chimene atumidwira, sadzabwerera kwa Iye chabe. Amapeleka zotsatira kuchokera kwa Iye amene wawatumiza. Mwa ichi, ngati mwakhala mukulandira mawu a Mulungu khulupilirani kuti tsiku lina adzabala zotsatira m’moyo mwanu.

Zilibe kanthu kuti mwakhala mnyengo yanu kwa nthawi yaitali bwanji. Ngati mwakhala mukulandira mawu a Mulungu ndinu otetezedwa. Mawu a Mulungunso ndi Mzimu, mwaichi amabala zotsatira zauzimunso. Iwo salemekeza malamulo a chilengedwe. Daliranibe mawu a Mulungu ndipo mudzaladira zotsatira zauzimu zimene zidzadabwitsa okuzungulirani . iwo adzalemekeza Mulungu wanu.

PEMPHERO

Atate wa kumwamba. Mu dzina la Yesu, zikomo chifukwa chakudalilika kwa mawu anu. Posayangánira nyengo zomwe ndikudutsamo, ndidzadalirabe mawu anu. Mawu anu ndi odalilira ndi oona. Ndine otsimikizika kuti Mawu anu ali ndi mphamvu yakusintha nyengo zanga zoonongeka.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso onani ndikukonda masamba athu a pa internet awa:

Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *