Dziperekeni ku Chitsogozo Cha Mzimu Woyera – Apostle Joseph Ziba

Dziperekeni ku Chitsogozo Cha Mzimu Woyera - Apostle Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 17 December 2018

Dziperekeni ku Chitsogozo Cha Mzimu Woyera NDI M’TUMWI JOSEPH ZIBA

Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe. Masalimo 32: 8

Muuzimu, chitsogozo chimatanthauza zinthu ziwiri: kulangizidwa ndi  kuwongoleredwa. Malangizo amatanthauza kuphunzitsidwa kapena kupeza chidziwitso m’nkhani inayake kapena malo ena ake. Pamene, kutsogoleredwa  kumakunikira pa momwe zinthu zikuyenera kuchitikira. Chitsogozo chimatchedwanso malangizo operekedwa mu mphindi yokhazikika.

Mulungu amatitsogolera m’njira zambiri monga pakuzindikira, pakukhudzidwa kwa mtima wathu, komanso pakumvetsetsa ndi kudziwa zinthu.

Mukuzindikira timagwiritsa ntchito ziwalo zathu zomwe ziri zofunika monga diso ndi khutu lauzimu. Umu ndi m’mene Mzimu Woyera zimamukhudzira potipatsa chitsogozo. Amakupatsani malangizo ndi chitsogozo kudzera m’maimvaimva auzimu.

Baibulo likunena za udindo wa Mzimu Woyera kuti: “… Iye adzatsogolera inu m’chowonadi chonse; pakuti sadzalankhula za iye yekha; koma chirichonse chimene adzamva, adzachilankhula; ndipo Iye adzakuwonetsani zinthu ziri nkudza” (Yohane 16:13). Mwachidule, Iye amakuchititsani kuti muwone kapena kumva zomwe Mulungu Atate akunena.

Ngati Mzimu Woyera akupitiriza kukutsogolerani izi ndi zomwe zidzakutsateni:

Ndipo AMBUYE ADZAKHALA WOSATHA, nadzakhutitsa moyo wako n’chilala, nadzathyola mafupa ako; ndipo udzakhala ngati munda wothirira, ndi ngati kasupe wamadzi, amene madzi ake satha (Yesaya 58:11).

Mwa kulankhula kwina, simudzalephera koma mudzakhutira ndi ubwino wa Mulungu: chipambano,  ndi zokondweretsa, zidzakhala moyo wanu.

PEMPHERO

Atate wopambana, zikomo chifukwa cha Mphatso ya Mzimu Woyera amene amakhala mwa ine. Mzimu Woyera wokoma ndikudzipereka ndekha kwa inu kuyambira lero. Nditsogolereni ndikundikupangitsa kuti ndichite zomwe Mulungu Atate amafuna kuti ndikhale. Mu dzina la Yesu, ameni.

 

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *