Khalani Owerengedwa – Mtumwi Joseph Ziba

Khalani Owerengedwa - Mtumwi Joseph Ziba

MBEU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 15 April 2019

Khalani Owerengedwa – Ndi Mtumwi Joseph Ziba

 

“Ndipo iwo adzaitanira bwanji pa iye amene sanamkhulupilira? Ndipo adzakhulupilira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji popanda olalikira?” AROMA 10:14 KJV

Nthawi zambiri enanu mumazitsekera kuchipinda kwanu nkumalilira Mulungu kuti apulumutse anthu. Izi nzoyenerezeka ndithu. Ndichabwino kumapemphelera miyoyo yotaika.

Komabe, pambali pa mapemphero anuwo, nzofunikira kuchitapo china choposera pamenepa. Vesi tawerengayi ikutionetsa njira yabwino yomwe Mulungu amapulumutsira anthu. Ndiyo kuwalankhula mau a Mulungu – uthenga wabwino wa Yesu Khristu. Choncho winawake wayenera kuti anyamure uthenga wabwinowu.

Njira yokhayo yomwe anthu angapulumuke ndipomwe amva uthenga wabwino wa Yesu. Ndipo m’kuona kwa Mulungu, ngodala zedi iye amene wanyamula uthenga wabwino kukafalitsa ku mayiko.

Kufotokozera za kudala kwa iye onyamula uthenga wabwino, Baibulo likuti:

“… Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino!’ . (Aroma 10:15).

Uzaniko wina lero za Uthenga Wabwino, ndi kuwerengedwa ngati m’modzi wa iwo apaderadera kwa Mulungu!

KUVOMEREZA

Ndine okonda miyoyo. Ndine onyamula uthenga wa zinthu zabwino. Kugawa uthenga wa Yesu Khristu ndicho chakudya changa cha tsiku ndi tsiku. Ndiikiza moyo wanga ndi zinthu zanga kufalitsa Uthenga Wabwino chifukwa ndi njira yokhayo Mulungu amapulumutsira otayika. Mu dzina la Yesu!

#ZitsimikizoZosalephera
#MoyoWosakanidwa

 

Pitanikuwebusaitiyathu: www.fountainofvictory.org

Komasotipezenipamasambaathuawa:
Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *