KUBZYOLA KWA MPHAMVU YA CHIKHULUPILIRO- MTUMWI JOSEPH ZIBA

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 8 April 2019
KUBZYOLA KWA MPHAMVU YA CHIKHULUPILIRO- NDI MTUMWI JOSEPH ZIBA
“…Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.” Marko 9:23
Mulungu watiika ife m’dziko la zosatheka (dziko lapansi) kuti tigonjetse zosathekazi. Ndipo Bayibulo likuta izi kudzera mwa chikhulupiriro ife tigonjetsa dziko la zosatheka (1 Yohane 5:4). Funso ndi loti: n’chani chapamwamba chokhudza chikhulupiriro kuti aliyense ali nacho amagonjetsa dzikoli?
Tawerengapo malo ambiri m`bayibulo mene munalembedwa kuti zonse ndizotheka ndi Ambuye. Monga, Mateyu 19:26, Mariko 10:27, Luka 1:37, Luka 18:37.
Koma vesi liri mwambamu ikubweretsa poyera chilungamo chofunikira. Ikunena kuti zinthu zonse n’zotheka kwa iye amene amakhulupirira (amene ali nacho chikhulupiriro); mene zililimo zinthu zonse nzotheka ndi Mulungu.
Izi zikuonetsera kuti chikhulupiriro chimamuyika munthu m`gawo la machitachita a Mulungu. Ndipo ngati Mulungu wapatsa inu chikhulupiriro, wakuthekeretsani inu kuchita zinthu monga Iyeyo. Lemekezani Mulungu.
Pamene chikhulupiriro chanu chikukula, momwemonso mochuluka mumagonjetsa zosatheka. Imvani Mau a Mulungu kwambiri ndipo chikhulupiriro chanu chidzakwera pakuti chikhulupiriro chidza pomva Mau a Mulungu (Aroma 10:10).
PEMPHERO
Atate wamtengo wapatali, ndikuthokoza kamba ka mwayi woti ndithe kugonjetsa zosatheka kudzera mwa chikhulupiriro, monga umo mumachitira. Kuyambira lero, ndikudzipereka m`kuwerenga ndikulingarila Mau anu kuti mukaikize chikhulupiriro chochuluka mwa ine chimene ndichigonjeso chomwe chimagonjesa dziko lapansi. M`dzina lamphamvu la Yesu. Amen.
#ZitsimikizoZosalephera
#MoyoWosakanidwa
Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org
Komaso tipezeni pa masamba athu awa:
Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational
Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba
YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg
Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate
Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate
Recommended Posts

Dalirani Mawu Ake – Mtumwi Joseph Ziba
May 27, 2019