Kugunda kwa Mtima wa Atate – M’tumwi Joseph Ziba

Kugunda kwa Mtima wa Atate - M’tumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 3 December, 2018

Kugunda kwa Mtima wa Atate – M’tumwi Joseph Ziba

Munthu ndani kuti mumkumbukila? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? Masalimo 8:4

Ndi chachidziwikire m’malembo oyera kuti Atate wathu wakumwamba amakonda miyoyo. Amalemekeza kwambiri munthu pa zolengedwa zonse.

Mawu oti “kum’kumbukira” mu vesi lapamwambalo akutanthauza “kukhazikiza koonekera”, “kupyoza” mu chikumbukiro, “kusangalala” ndi “kuganizira”. Izi zikusonyeza kuti kugunda kwa mtima wa Mulungu ndi malingaliro ake pa munthu aliyense ndikofanana; posawerengera kuti ndi mkhristu kapena ayi. Palibe amadziwa mtengo kapena kulemelera kwa munthu kupatula Mulungu.

N’zosadabwitsa kuti amakhumba kuti munthu aliyense apulumuke ndikufika podziwa choonadi (1 Timoteyo 2:4). Ngakhale zili choncho, Iye sangatsike pansi kudzalalikira miyoyo yotayikayo; anasiya lamulo lofalitsa uthenga wabwino wa Yesu Khristu kwa inu ndi ine.

Njira yotsimikizika yosunthira mtima wa Mulungu ndikufikira miyoyo. Muonetsereni Mulungu kuti mumamukonda, pakukonda chomwe iye amachikondetsetsa. Chitani chomwe mungathe pa kugwiritsa ntchito zomwe mulinazo pakufikira miyoyo. Mukachita izi, Atate wanu wakumwamba azakondwera.

PEMPHERO

Atate wokondedwa amene muli kumwamba, zikomo pondiululira khumbo la mtima wanu. Mumakonda miyoyo kuposa zolengedwa zonse. Ndikudziikiza ndekha pakufikira miyoyo chifukwa ndi njira yotsimikizika yoonetsera chikondi changa chakuya kwa inu m’dzina la Yesu. Amen.

Zatengedwa pa “Kugunda kwa Mtima wa Atate” mutha kupeza uthenga wonse poimba nambala iyi +265(0)888114374

#Zitsimikizo zosalephera#
#Moyo wosakanizidwa#

Tsamba pa intaneti: www.fountainofvictory.org

Tsamba la fesibuku: https://www.facebook.com/fovchurchinternational
https://www.facebook.com/pastorjosephziba

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *