Kupanda Mphamvu Kwa Themberero Pa Moyo Wanu – Mtumwi Joseph Ziba

Kupanda Mphamvu Kwa Themberero Pa Moyo Wanu - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 4 February 2019

Kupanda Mphamvu Kwa Themberero Pa Moyo Wanu – Mtumwi Joseph Ziba

“Chifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,” 2 Akorinto 5:17 BL92

Akhristu ena, kamba kakusamvetsetsa chimene ali mwa Khristu, sagona tulo akaganiza za matembelero akumtundu pa moyo wawo. Uwamva ena akuti, “Malonda, banja , komanso ntchito yanga sizikuyenda. Izitu n’zomvetsa chisoni kotheratu.

Pa mwana wa Mulungu, themberero laku mtundu siliphula kanthu. Ngati uli wobadwa mwatsopano, ndiwe wopatulika ku izi ndipo moyo wako ukuyenera kukhala wopita chitsogolo.

Lemba lathu lotsegulira likuta yense ali mwa Khristu ali chipango chatsopano. Mawu oti “chipango kapena cholengedwa chatsopano” amatanthauza cholengedwa chimene kunalibeko kale lonse. Ndiye, zingatheke bwanji, cholengedwa chatsopanochi kusautsidwa ndi matembelero omwe gwero lake ndi makolo omwe adatisiya kale lomwe? Izi n’zosatheka mpang’ono pomwe.

Lembali likutinso “…zakale zapita…”. Izi zikuphatikiza ma kulumukizana kulikonse komwe mudali nako kale musadabadwe mwatsopano. Matemberero akumtundu, umphawi, kusabereka, nthenda zoyamwira monga Khasa, Kuchepa/Kuchuluka kwa sugar thupi, Mphumi, Kuthamanga kwa mtima ndi mavuto a m’bongo, ndi zina zotero – zonsezi zapita; chifukwa ndinu obadwa mwatsopano.

Potsiliza lemba likuti, “…taonani, zonse zakhala zatsopano” kutiuza kuti chilichonse chokhudzana ndi munthu wobandwa mwatsopano (kapena kuti mKhiristu) ndi chatsopanonso. Zonsezi zimayambika pamene munthu walandira Yesu ngati Mbuye ndi Mpulumutsi wa moyo wake.

N’zosadabwitsa kuti Mtumwi Paulo mwa chitsogozo cha Mzimu Woyera akufotokoza za cholengedwa chatsopano momveka bwino ku Aefeso 2:10. Iye akuti, “Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m’menemo.”

Inde, ndife ntchito ya manja ake a Mulungu, cholengedwa chopangidwa ndi Mulungu chimene sichikhudzidwa ndi matemberero a ku mtundu.

PEMPHERO
Tate wakumwamba, tikuthokoza za kuwunika kwa m’mawu anu. Zikomo potsegula maso anga kuti ndiwone za chilengedwe changa chatsopano. Ndikuvomera za chimene ine ndili ndipo ndiyenda m’kuzindikira kwa ichi. Ndipo ine sindingazunzike ndi matemberero aku m’badwo. M’dzina la Mphamvu la Yesu, Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *