Lunjika pa Zomwe Zili Zothandiza – Mtumwi Joseph Ziba

Lunjika pa Zomwe Zili Zothandiza - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 20 May 2019
Lunjika pa Zomwe Zili Zothandiza – Mtumwi Joseph Ziba

“Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” Machitidwe a Atumwi 4:12 (Buku lopatulika)

Chipulumutso sichichokera ku ntchito zimene tichita, kapena pakumvera malamulo, kapena tsiku lomwe timapephera, kapena pa malo okumanilako polambira. Sichimabwera pakuvomereza machimo athu kwa Mulungu, kapena pakudzimvera chisoni pa machimo athu. Chipumumutso chimabwerapa kukhulupilira ndi kuvomereza Umbuye wa Yesu Christu (Aroma 10:9-10).

Mwaichi, mfundo zathu ngati a Khristu zisamakhazikike pa za masiku opembedza, kapena pa za kumvera chilamulo cha Mose, kapena ngati timapembedzera mkachisi kapena pa mtetete. Izi ndi zinthu zazingóno. Nkhani yeniyeni yagona pa Khristu (Akolose 2:17).

Chidwi chathu chachikulu chikhale kuona ngati Khristu akulalikidwa. Pakuti ngati sitilalikira za Khristu, anthu sangathe kupulumuka.

PEMPHERO
Atate wa kumwamba, tikuyamika chifukwa cha mphatso ya dzina la Yesu. Tapulumuka kupyolera mwa Iye. Tipatseni Kulimbika mtima kuti tilalikire za Iye ndi mtima onse komanso mosaopa. Mudzina la Yesu. Ameni.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso onani ndikukonda masamba athu a pa internet awa:

Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *