Mawu a Mulungu, amagwira ntchito nthawi zonse – M’tumwi Joseph Ziba

Mawu a Mulungu, amagwira ntchito nthawi zonse - M'tumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 1st April, 2019

Mawu a Mulungu, amagwira ntchito nthawi zonse – Ndi M’tumwi Joseph Ziba

Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza chifukwa, pamene mudalandira mawu a Mulungu, amene mudawamva kwa ife, simudawalandire monga mawu a anthu, komatu monga ali chowonadi ndithu, mawu a Mulungu amenenso agwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. 1 Atesalonika 2:13

Mu vesi yotsogolera pamwambapo, mawu oti “agwira ntchito”akutanthauza “ochitachita” kapena “amphamvu”. Izi zikutanthauza kuti nthawi iliyonse imene muwerenga kapena kukhala pamene pakulalikidwa mawu a Mulungu china chake chimachitika ndi inu: pali chochitika cha mphamvu kudzera mukugwira ntchito kwa mawu a Mulungu. Pali kuumbidwa kapena kusinthika pa moyo wanu ndi nyengo zanu munthawi ya ulemelero ngati iyi. Choncho musadzikanize mkutumikilidwa kwa mawu a Mulungu.

Izi zikutanthauza kuti mutha kusintha nyengo iliyonse yosafunikira mmoyo mwanu pakuikiza mawu a Mulungu olingana ndi nyengoyo muuzimu mwanu, kuwayankhula kapena kuvomereza mawu amphamvu ku nyengo imeneyo.
Ndinu ovutika? Muli ndi matenda a khansa, Edzi kapena nthenda iliyonse? Kodi muli ndi mavuto a kusautsika mmaganizo? Kodi bizinesi yanu kapena ntchito yanu siikuyenda? Muli ndi mfungulo mmanja mwanu: ziikizeni nokha mkuwerenga kapena mkulalikidwa kwa mawu a Mulungu okhuza nyengo yanu ndipo muvomereze. Mukatero, nyengo zanu zisinthika chifukwa mawu a Mulungu amagwira ntchito nthawi zonse.

CHIVOMEREZO
Ndimakonda mawu a Mulungu. Palibe chingandisokoneze. Ndimagwiritsa ntchito mawu a Mulungu ngati lupanga pomenya nkhondo ndipo zimagwira, mchifukwa chache ndimachoka muchigonjetso mkupitanso muchigonjetso. Mudzina la Yesu. Ameni.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso tipezeni pa masamba athu awa:
Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *