M’malo modera nkhawa, Lingalirani – M’tumwi Joseph Ziba

M’malo modera nkhawa, Lingalirani - M'tumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 11th February, 2019

M’malo modera nkhawa, Lingalirani – Ndi M’tumwi Joseph Ziba

Ndipo ndani wa inu ndikudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wache mkono umodzi? Mateyu 6:27

Chimodzi mwazinthu zomwe mukuyenera kupewa ndi kudera nkhawa ngati mufuna chipambano chachikulu mu chaka chino.

Kudera nkhawa kumachepsya mzimu wanu. Mwaichi, mumalephera kukwaniritsa zinthu zazikukulu chifukwa mumasowa kukonderedwa kwa Mulungu amene sapezeka m’malo mophinjika, koma a chimwemwe

Inu mukuyenera kulingalira. Kulingalira ndi ndondomeko younikira maganizo ndi zinthu zina pofuna kupeza mayankho. Izi ndizo Mulungu amafuna. Mwaichi, amayembekezera kuti inu muzipeza nthawi yolingalira.

Podera nkhawa, umaganizira zinthu zomwe zimakuwopsya. Izi zimabweretsa mantha ndikuika mafunso ndi zotsamwitsa zimene simungapeze mayankho m’maganizo mwanu. Izi, Mulungu amadana nazo.

Ngati pali chinthu chimene mwakhala mukuchilingalira koma simunapeze yankho chisiyeni. Chitha kukhala chizindikiro choti sizikuyenera kukhala m’malingaliro anu.

Ine sindimakhala pa mpanipani; ndimadziwa zinthu zimene zili m’kuthekera kwanga ndipo ndimalingalira pa izo. Ngati pali china chondikulira ndimachitengara kwa Mulungu Atate mu pemphero ndi kuchisiya.

Osamwalira mwachangu chifukwa choganizira zinthu zimene simukuyenera kuganizira. Kumaukonda moyowu ndipo uchengetereni.

Chibvomerezo:
Ine sindidera nkhawa, koma ndimazitaya nkhawa zonse kwa Ambuye. Nkhawa sizanga; kulingalira ndikwanga. Ndimalingalira mayankho, sindidzayesa kuganizira zinthu zomwe sindidzapeza mayankho ake. Munjira iyi ndidzakhala moyo wachimwemwe masiku onse amoyo wanga;posaganizira zanyengo za moyo. Mu dzina la Yesu, Amen.

 

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *