Mpangitseni Mulungu kukhala nanu ngongole – Mtumwi Joseph Ziba

Mpangitseni Mulungu kukhala nanu ngongole - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 25 March 2019

Mpangitseni Mulungu kukhala nanu ngongole – Mtumwi Joseph Ziba

“Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.” Masalimo 50:23 (Buku lopatulika)

Ambiri amamtamanda Mulungu pa zimene wachita: zomwe nzabwino ndithu. Koma, palinso chinsinsi china chomupangitsa Mulungu kuti alowelele m’zochitikiza za moyo wanu, chimene chili kupereka matamando awuneneli kwa Iye.

Matamando awuneneli amaperekedwa kwa Mulungu pa zinthu zimene sadachite. Mukamtamanda Mulungu pa zimene sanachite, mumampangitsa kukhala nanu ngongole. Iye safuna kukhala m’ngongole nkana amadza ndikudzachita chimene inu mukumtamandira.

Mukawerenga 2 Mbiri 20, mumvetsetsa zimene ndikunena. Pamene mafumu atatu adakathira nkhondo kwa mfumu Yehosophati waku Yudeya, anthu akuYuda anayamba kupereka matamando awuneneri. Ndipo zotsatira zake zinali zosayembekezereka: adani awo anakanthana okha-okha.

Ndipo, m’zonse zimene mukudutsamo kapena mukufuna Mulungu akuchitireni, mtamandeni m’zimenezo zisanachitike. Mukatero muwona dzanja lake la mphamvu likudza kudzakuthandizani ndikukupatsani izo mufuna.

PEMPHERO
Atate wakumwamba, zikomo chifukwa simufuna kukhala m’ngongole. Potero, ndikutamandani m’masiku onse a moyo wanga; posatengera kuti mwachita kapena ayi. Moteromo, ndidzayenda mosalekeza m’chipambano chanu. Mu Dzina la Yesu. Amen.

 

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso onani ndikukonda masamba athu a pa internet awa:

Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *