Mphatso ya Nthawi – Mtumwi Joseph Ziba

Mphatso ya Nthawi - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 22 April 2019
Mphatso ya Nthawi – Mtumwi Joseph Ziba

“Chitani machawi, popeza masiku ali oipa.” Aefeso 5:16

Anthu ena amaona ngati nthawi ndikusuntha kwa muvi wa otchi. Uku nkusamvetsetsa chabe komwe kwapangitsa anthu ambiri kusagwiritsa ntchito bwino nthawi. Zotsatira zake amalephera kukwaniritsa zazikulu zomwe Mulungu amafuna kuti iwo akwaniritse.

Ndi Mulungu amene analenga nthawi (Genesis 1:14). Komanso bayibulo limanena kuti Mulungu amasintha nthawi (Daniel 2:21). Izi zikutanthawuza kuti sanangolenga nthawi komanso amayilamulila.

Tsono, muyitenge nthawi ngati mphatso yochokera kwa Mulungu pakupezeka kwnanu. Itengeni ngati mpata wakupezeka kwanu pa dziko pano wopatsidwa ndi Mulungu. Choncho igwiritseni nchito bwino.

Choncho musawononge kupezeka kwanu padziko pano ndikudandaula, mantha, kapena zoyipa zina zosamuyenera mkhristu. Koma, igwiritseni ntchito mzinthu zabwino zimene Mzimu Woyera akukutsogolerani kuti muchite. Moteromo mudzakhala moyo wokondwera ndi wopindulitsa kwa Mulungu ndikwa munthu.

PEMPHERO

Zikomo Atate chifukwa cha mphatso ya nthawi. Ndithandizeni mwa chitsogozo cha Mzimu wanu kuti ndiyigwiritse ntchito mwa nzeru tsiku ndi tsiku. Mu Dzina la Yesu Khristu, Amen.

 

#ZitsimikizoZosatsutsika
#MoyoWosakanizidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso onani ndikukonda masamba athu apa internet awa:

Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Comments

  1. Aaron Khundu : April 24, 2019 at 7:29 pm

    Izi ndi za mphamvu

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *