Muuzeni Tsatanetsatane wa Zomwe Inu Mukufuna –  Mtumwi Joseph Ziba

Muuzeni Tsatanetsatane wa Zomwe Inu Mukufuna -  Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 11 March 2019

Muuzeni Tsatanetsatane wa Zomwe Inu Mukufuna –  Mtumwi Joseph Ziba

Musati mudandaule kapena kukhala ndi nkhawa iliyonse, koma muzochitika zonse ndi muzonse, mwa pemphero ndi pembedzero (zopempha zenizeni), ndi kuyamika, mupitirize kumdziwitsa Mulungu zofuna zanu. Afilipi 4: 6 AMP

Ndidamvapo mbiri yopatsa chidwi ya munthu wina wotchuka wa Mulungu wa nthawi yathu ino. Pazaka zoyambirira za utumiki wake, iye adakhulupirira Mulungu kuti ampatse mpando woti azikhalira m’ofesi yake. Lingaliroli adalitengera kwa Mulungu m’pemphero. Nthawi iliyonse akamapemphera, iye ankati “Ambuye, ndipatseni mpando wa muofesi yanga”. Anachita zimenezi kwa pafupifupi chaka chimodzi ndipo Mulungu ankawoneka kuti sakuyankha.

Atatopa kupemphera moteremu, adati kwa Mulungu: “Ambuye, zikuwoneka kuti simukufuna kundiyankha pemphero langa; Choncho, sindikupemphaninso kuti ndikhale ndi mpando wa mu’ofesi “. Yankho la Mulungu linali losangalatsa. “Ndakhala ndikumva pemphero lako loti ukhale ndi mpando wa m’ofesi koma sindinadziwe kwenikweni mtundu wa mpando womwe ukuufuna – siunandipatsepo ndondomeko: kukula, mtundu, kapangidwe ndi zina zotero. Umayembekezera kuti ndikupatse chiyani? “

Munthu wa Mulungu analapa ndikufotokozera tsatanetsatane wa mpando umene adafuna ndipo Mulungu adampatsa. Mulungu alemekezeke!

Mulungu ndiye mwini dziko lonse koma adapatsa chifuniro kwa anthu kuti asankhe zomwe akufuna kwa Iye. Iye samakupatsani inu chirichonse: Iye amakupatsani inu zomwe inu mukuzipempha. Palibe zodabwitsa kuti lemba loyambirira pamwamba likunena kuti muyenera kumupempha momveka bwino mukamapemphera.

Baibulo limafotokoza kuti Mulungu ndi Atate wabwino amene amadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana ake (Mateyu 7:11). Komabe, kwa Iye, mphatso yabwino ndi yomwe mumalandira pambuyo pofunsa.

PEMPHERO

Wokondedwa Atate, Inu mwatsegula maso anga ku zomwe Inu mukufuna kuti ine ndizichita pamene ine ndikupemphera. Kuchokera lero, ndikhala ndikufotokoza mwatsatanetsatane zomwe ndikufuna ndipeze kuchokera kwa Inu monga momwe mukufuna, m’dzina la Yesu Khristu. Ameni!

 

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *