Ndizoposera Chilimbikitso – Mtumwi Joseph Ziba

Ndizoposera Chilimbikitso - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba. 18 March 2019
Ndizoposera Chilimbikitso – Mtumwi Joseph Ziba

Machitidwe atumwi 20:32
Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa Mau a cisomo cace, cimene ciri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu colowa mwa onse oyeretsedwa
Anthu ena amaoneka kuti samvetsetsa bwino phindu la kukhala pansi pa utumiki wa mawu a Mulungu. Umawamva akuwauza anzawo akamapita ku kumapemphero : “sitipita ku tchalitchi lero; mukangotipempherera.” Ndipo amapitiriza ndikuti, “matupi athu sangapezekeko koma tili nanu limodzi mumzimu.” Kulakwitsa kwakukulu! Akanadziwa anthu amenewa phindu lakuzionetsera pamaso pa Mulungu ndi kukhala pansi pa ulaliki ndi chiphunzitso cha Mau ake, akanaganiza kawiri asanapange chiganizo chosakapezeka mumkumano wa tchalitchi.
Kulalikidwa ndi kuphunzitsidwa kwa Mau a Mulungu sikuti ndikongopereka chilimbikitso-ndikoposa chilimbikitso. Ndikudziwa anthu enanu mumakonda kuwerenga mabuku achilimbikitso ndiponso kumvetsera zokamba za anthu okonda kulimbikitsa zimene ndizabwino. Komabe, mukuyenera kudziwa kuti anthu okamba zopereka chilimbikitso ndi makumbu okamba zolimbikitsa amakhala ndi malire; amangokamba zokhudza malingaliro koma sakhudza mzimu wamunthu womwe ndi weni-weni. Ndicho chifukwa chake sangakusintheni inu: amangoonjezera mzeru mwainu. Umu sindimo achitira Mau a Mulungu.
Lemba lotsegulira mwambamu mokongola, likuonetsera modabwitsa zilungamo ziwiri zokhudza Mau a Mulungu ndi zomwe amachita kwa ife:
Mau ali “…ndi mphamvu yakumangirira…” Mu Mau ena, amakuza kapangidwe mwainu ndipo imatulutsa munthu wonga Mulungu- imapanga chifanifani changwiro cha Mulungu mkati mwa inu poti Mau a Mulungu ndiwo Mulungu amene. Imatulutsa mwainu munthu amene Mulungu anakupangani kuti mukhale. Mau ndi mzimu ndipo ukawamva , amatumikira mu mzimu wanu ndipo amausintha.
Ndikhulupirira sichachilendo kumva kuti muli ndi cholowa mwa Khristu, si choncho? Baibulo limanena motsimikiza mu lemba lina kuti Mulungu anatipanga ife okwanira kapena oyenera kukhala atenga mbali a cholowa cha oyerawo mu kuwala (Akolose 1:2). Funso mkumati: kodi munthu angalandire kapena kutenga cholowa chimenecho? Kapena munthu angapeze bwanji katundu wa m`nyumba ya Mulungu, Atate wawo?
Apa ndipomwe Mau a Mulungu amatenga nawo gawo. Lemba liri mwambali likutinso Mau ndiothekera “kupatsa inu cholowa…” Mwa mawu ena Mau a Mulungu amakwanitsa kuwombora kwa inu icho Mulungu wakusungirani inu. Ndi chopatsira cholowa cha Mulungu kwa ana ake. Ndiye mongoyankhula, kweni-kweni, zimene Khristu anakwanilitsa kwa inu monga, kulemera; thanzi la umulungu; kuomboredwa, pongotchula zochepa, zimaperekedwa kwa inu kudzera mu utumiki wa Mau.
Kulitsani chizolowezi chokonda chiphunzitso, ulaliki ndi kuwerenga Mau a Mulungu lero ndipo muona moyo wanu ukusuntha kuchoka ku ulemerero kunka ku ulemerero wina m`dzina la Yesu.

PEMPHERO

Atate wamtengo wapatali, zikomo kwambiri poonetsera kwa ine chuma cha Mau anu. Ndikudzipereka kuwerenga Mau anu tsiku liri lonse ndipo sindijomba kutchalitchi m`chaka chimenechi; pakuchita izi, moyo wanga ukasuntha kuchoka ku ulemero kunka ku ulemerero wina ndinso kuchoka kuchipambano kunka kuchipambano china m`dzina la Yesu!

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *