Ndopa Izi Zikukhozga Phangano la Sono – Wakutumika Joseph Ziba

Ndopa Izi Zikukhozga Phangano la Sono - Wakutumika Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 13 May 2019
Mwazi wa Chipangano cha Tsopano – Mtumwi Joseph Ziba

“pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.” Mateyu 26:28 (Buku lopatulika)

Aroma 8 vesi 3 imati chilamulo chinafooka mwa thupi. Mwaichi, Mulungu analingalira zokhozanso ufooko umenewu pokhadzikitsa chipangano cha tsopano ndi ife. Yesu Christu ndiye mkhala pakati wa chipanganochi.
Vesi lotsogoleralo lafotokoza choonadi cha mwazi wa mkhala pakati wathu. Likuti uwu ndi mwazi wa pangano. Kodi izi zitanthauzanji?

Mwazi wa Yesu umagwrira ntchito mu njira ziwiri izi:

Choyamba, umavomereza Chipangano cha Tsopano. Mwazi wake umasonyeza kuti Chipangano cha Tsopano chikugwira ntchito. Mwa ichi, mawu aliwonse amene Mulungu analankhula kwaife ali akuchitachita.

Chachiwiri, Uikira umboni pa imfa ya Yesu. Mwaziwu umaikira umboni kuti pangano lathu Yesu, anatifera. Mwaichi, titha kutenga chilichonse chomwe Mulungu Atate wathu anatisungira mwaufulu.

Chilungamo, Kuyeretsedwa, Kuomboledwa, madalitso, nzeru, thanzi labwino, mtendere, chuma ndi zina zotero ndi zolowa zathu za muyaya. Ngati Satana ayesa kukuvutitsani kumbali iliyonse muzinthu zimenezi, mkumbutseni za mwazi wa Chipangano cha Tsopanochimene chinakugulirani zonse.

CHIVOMEREZO
Zikomo Ambuye Yesu pokhetsa mwazi wanu chifukwa cha ife. Nsembe yanu yatithekeletsa kupeza chuma chamtengo wa patali cha Mulungu Atate ngati ana olowa mnyumba.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org

Komaso onani ndikukonda masamba athu a pa internet awa:

Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *