Ntchito: Bwalo Lomwe Mulungu Amazionetserapo – Mtumwi Joseph Ziba

Ntchito: Bwalo Lomwe Mulungu Amazionetserapo - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 4 March 2019
Ntchito: Bwalo Lomwe Mulungu Amazionetserapo – Mtumwi Joseph Ziba

Mbeu yammunda iliyonse isadakhaleko pa dziko, chitsamba chammunda chirichonse chisadamere: Pakuti Yehova Mulungu anali asadapangitse kuti mvula igwe pa dziko lapansi, ndipo padalibe munthu oti atipule nthaka. Genesesi 2:5

Chaputala choyamba cha buku la GenesisI. lkulongosora za kulengedwa kwa dziko. Likufotokoza m’mene Mulungu analengera kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zokhalamo. Kudabwitsa kwake, muzindikira kuti zimene Mulungu akulenga sizikupezeka padziko lapansi – zonse zomwe zinalengedwa zikuonetseredwa kaye muuzimu. Izi zikukambidwa mu gawo loyamba mu vesi ya pamwambayo. Koma nchifukwa chiyani zinali choncho?

Baibulo likunena kuti chifukwa “AMBUYE Mulungu anali asadapangitse kuti mvula igwe …… ndipo KUTI PADALIBE MUNTHU OTI ATIPULE NTHAKA.”

Liwu loti “Kutipula” lomwe lili mundime yomwe tawelengayi likutanthauza “kugwila ntchito”. Choncho, zomwe Mulungu adalenga sizikadaonekera pa dziko lapansi pakuti padalibe munthu woti agwile ntchito.

Dziwani ichi, kwa mwana wa Mulungu, ntchito sikupanga ndalama kokha ayi, koma ndi ngati bwalo loti Mulungu azionetsere yekha. Ntchito imakhala ngati bwalo lomwe Mulungu amagwiritsa ntchito kuonetsera chisomo chake, madalitso komanso kudzodza pa moyo wanu. Izi zikutanthauza kuti mukapanda kupeza ntchito yogwira, sikuzatheka kuti muonetsere mphamvu ya Mulungu mu gawo lilironse la moyo wanu.

Ndiye nchifukwa chake musamalore m’dyelekezi kuti akulepheretseni kugwila ntchito. Monga mwana wa Mulungu musamangokhala manja lende. Mukuyenera kulembedwa ntchito, kuyamba bizinesi kapena kuyamba sukulu ndi zina zotero, nkuchita zinthuzo molimbikira. Mukatelo muzatokosola madalitso, chisomo, kukondeledwa ndi kudzodza kwa Mulungu kuti kubwere pa njira yanu.

PEMPHERO

Atate wabwino, mu dzina lamphamvu la Yesu Khristu, zikomo chifukwa cha nzeru kuchokela ku mawu anu. Mwatsegula maso anga, ndipo kuyambila lero mpaka mtsogolo. Sindikhala wa manja lende kapena kuchita ulesi pa ntchito yanga. Ndizagwila ntchito molimbikira m’masiku onse podziwa kuti ntchito ndi bwalo lomwe inu Mulungu mumazionetsera nokha. Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *