Ntchito zanu zidzakutsatani – M’tumwi Joseph Ziba

Ntchito zanu zidzakutsatani - M'tumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 18 February, 2019

Ntchito zanu zidzakutsatani – M’tumwi Joseph Ziba

Ndipo ndinamva mawu ochokera kumwamba, nandiuza kuti, lemba, Odala akufa omwe amwalira mwa Ambuye. Kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; ndipo ntchito zawo ziwatsatira.
Ndikufuna muyang’anitsitse lemba lili m’mwambamu kachiwiri. Chivumbulutso 14:13

Lembali silikungonena kuti “Odala akufa omwe amwalira mwa Ambuye…” likupitilira kunena kuti “…akapumule ku zolemetsa zawo; ndipo ntchito zawo ziwatsatira”. Izi zikutanthauza kuti, sialiyense amene amwalira mwa Ambuye ali odala. Ndi okhawo amene achita ntchito za Ambuye omwe ali odalitsika ndithu.

Vesiyi yanenetsanso kuti “ntchito zawo zizawatsata, iwo akumwalira mwa Ambuye”. Funso nali: ngati mutamwalira lero, ndi ntchito zanji zingakutsateni kumwamba?

Pamene mukugwira ntchito zanu zatsiku nditsiku monga za mu ofesi, ma bizinesi, kuchita zamaphunziro, ndi zina Zotero, osaiwala kuchitanso ntchito za Ambuye. Khalani anzeru ndipo nthawi yanu igaweni bwino tsiku lirilonse kuti musalephere kuchita ntchito za Ambuye pakuti ndizo zidzakutsateni osati zolemetsa zanuzo ayi.

Ntchito zanu zidzakuikirani umboni pamaso pa Mulungu wamphamvu zonse; kunena kuti, “anthu anapulumutsidwa chifukwa cha iye”, “ameneyu ankapemphelera kufalitsika kwa uthenga wabwino mene anali pa dziko lapansi”, ndi zina Zotero; mwaichi Mulungu akakupatsani mphoto moyenelera.

Osakhala moyo wachitaiko. Fufuzani ngati izo mukuchita tsiku ndi tsiku zidzakutsateni kumwamba. Yendetsani moyo wanu monena kuti ukhale chokukonzekeretsani chabe ku mmoyo wamuyaya.

PEMPHERO
Atate wakumwamba, zikomo pondipatsa nzeru zokhalira tsiku nditsiku. Ndikuzindikira kuti moyo padziko lapansi ndi waufupi; ndipo kuti pali moyo wina umene ulinkudza. Ndikukana kukhala moyo wachitaiko mmasiku anga okhalira pano pa dziko pansi. Mwaichi ndikulonjez kuti moyo wanga ndi zinthu zanga zidzachita ntchito zimene munaika mnjira yanga pakuti dzadziwa tsono kuti ntchito zimenezi ndizo zidzanditsate. M’dzina la mphamvu la Yesu, Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *