Nyumba ya Mulungu: Malo osulila chipambano – Mtumwi Joseph Ziba

Nyumba ya Mulungu: Malo osulila chipambano - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 5 January 2019

Nyumba ya Mulungu: Malo osulila chipambano – Mtumwi Joseph Ziba

”Koma iwe Betelehemu Efurata, ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda, mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzalamulia Israeli, amene chiyambi chake n’chakalekale, n’chamasiku amakedzana.” Mika 5:2 CCL

Pamene chaka chatsopano chikuyamba, ambiri amakhala ndi zokhumba zabwino m’malingaliro awo. Amakhala ndi njira zambiri za momwe angakwanilitsire malingaliro awowo. Izi n’zabwino, koma njira yokhayo imene ungakwanilitsire zokhumba zako ndikuchilimika pomvetsera mawu a Mulungu.

Lemba lotsogolera likukamba za olamulira wamkulu waku Betelehemu, m’Israeli. Mbiri ya Bayibulo imafotokoza za msalamangwe amene anabadwira kapena kupanga mbiri ku Betelehemu. Mwa chitsanzo, Yesu Khristu, Mfumu Davide, Mfumu Solomoni ndi ena ambiri (2 Samuel 5:9 ndi Luka 2:4. Betelehemu anali malo awuneneli.
Liwu lakuti “Betelehemu” likuchokera ku mawu awiri achi Heberi otanthawuza kuti “Nyumba ya mkate”. Mkate ukuyimilira mawu a Mulungu. Betelehemu anakonzedwa kuti ndi kobadwira mafumu ndi atsogoleri.
Mu chipangano chatsopano, Betelehemu ndi nyumba yomwe choonadi cha Mulungu chimatumikilidwa (1 Timoteyo 3:15).
Ngati mukukhumba kukhala msalamangwe, onetsetsani kuti chaka chino musamajombe ku tchalitchi. Kadyeni mkate m’nyumba ya Mulungu ndipo moyo wanu udzatumphuka m’ukulu.

PEMPHERO

Atate wathu wakumwamba, ndikuyamika chifukwa cha kuwunikira kochokera m’mawu anu. Ndawona kuti kupezeka m’nyumba yanu kumene chowonadi chimatumikiridwa ndicho chinsisi cha ukulu wanga. Ndidzakhala okondwera ndipo sindidzajomba m’mikumano ya mpingo m’chakachi. Mawu a Davide akhala nyimbo yanga, “Ndinasangalala m’mene ananena nane, tiye ku nyumba ya Yehova”. Mu dzina la mphamvu la Yesu, Amen.

#Zitsimikizo Zosalephera
#Moyo Wosakanidwa

#ApostleJosephZiba #FountainofVictory  #InfallibleProofs #LifeUndenied

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *