Pemphererani Atsogoleri Anu – Mtumwi Joseph Ziba

Pemphererani Atsogoleri Anu - Mtumwi Joseph Ziba

MBEWU ZACHIPAMBANO – Lolemba, 6 May 2019

PEMPHERERANI ATSOGOLERI ANU – NDI MTUMWI JOSEPH ZIBA

||1 Timoteo 2:1-2||

Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse; 2cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m’moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monse.

Pa zifukwa zosiyanasiyana ena saona chifukwa chopempherera ulamuliro. Amaganiza kuti atsogoleri safunikira athu.

Komabe, m’lemba liri mwambali, mtumwi Paulo ndichitsogozo cha Mzimu Woyera akubwereza kufunikira kopempherera atsogoleri athu. Akuti pemphererani aliyense MAKAMAKA a maudindo kuti mukhale Moyo wa bata ndi mtendere.

Atsogoleri amaikiza tsogolo ndi kayendedwe ka banja, mpingo, dera ndinso m’dziko lonse. Baibulo limati ndizakantha Mbusa ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu. (Onani Zekariya 13:7, Mateyu 26:31). Ngati atsogoleri atayika ndithudi tonse tatayika. Choncho nkoyenereka kuwapempherera kuti Mulungu awapatse nzeru ndi chitsogozo atsogoleri munjira yomwe akufuna kuwatsogolera.

PEMPHERO

Ambuye wopambana, zikomo pondipasa atsogoleri m’mpingo, m’banja, kusukulu, kuntchito, m’dera ndi m’dziko lonse. Apatseni kumvetsetsa ndi nzeru ndikuti atitsogolere ndi kutilondolera ife kukuopani inu. M’dzina la Yesu. Amen

#ZitsimikizoZosalephera
#MoyoWosakanidwa

Pitani ku webusaiti yathu: www.fountainofvictory.org,

Komaso tipezeni pa masamba athu awa:
Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *