Sema Dziko Lako – Mtumwi Joseph Ziba

Sema Dziko Lako - Mtumwi Joseph Ziba

MBEU ZA CHIPAMBANO – Lolemba, 29 April 2019
Sema Dziko Lako – Ndi Mtumwi Joseph Ziba

” Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pache pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika olowa nyumba wa zonse, mwa iyenso analenga maiko ndi am’mwamba omwe.” Ahebri 1:1-2 KJV

Tikukhala m’masiku ovuta omwe palibe chomwe chikuyenda monga zifunikira. Kuli nkhondo, uchifwamba, milili ya matenda, njala, kuipa mtima ndi kuvuta kwa zachuma. Za m’bado uno, Baibulo likutsindika motere , “Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu (Yesaya 60:2).

Ngakhale zili chonchi, chiyembekezo chidakalipo kwa mwana wa Mulungu kukhala opatulidwa ku izi. Lemba tayamba nalo mwambamu lija likutitsimikizira kuti Mulungu analenga dziko ndi miyamba kudzera mwa Mbuye wathu Yesu.

Liwu loti “Miyamba” mu lemba limeneli linatanthauziridwa kuchokera mau a mu chi giriki oti “Aions”, omwe amatanthauza nyengo ya nthawi komanso njira ya moyo ndi zochitika.

Izi zikutanthauza kuti inuyo monga m’khristu, Miyamba yanu siimagwedezeka ndi zokuzungulirani mu dzikoli. Miyamba yanu ili m’manja mwa Yesu Khristu.

Tsono poti mwadziwa choonadi chi, mukuyenera kuchita chiyani? Baibulo likunena kuti miyamba inasemedwa ndi mau a Mulungu (Ahebri 11:3).

Choncho, ngati wadutsa mu nyengo yotsutsana ndi zomwe Mulungu anena, ndi udindo wako kuipanga nyengoyo ibwelere kudzera m’kulankhula mau odzadza ndi chikhulupiliro.

Inde, utha kuchotsapo zina nuikapo zina, kupeleka maonekedwe omwe ufuna, kapena kuibweza nyengo iliyonse. Uku ndiye kusema nyengo yako pogwiritsa ntchito kamwa lotsogozedwa ndi Mzimu. Baibulo limanena kuti, “Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nkunena kuti ‘Akwezeni’”, ndipo mwaichi moyo wako udzayenda njira yosiyana ndi ya dziko lapansi.

KUVOMEREZA

Kamwa langa ndilodalitsidwa. Kamwa langa ndilodzodzedwa ndi Mzimu wa Mulungu. Ndimaligwilitsa ntchito kukonza njira ya moyo wanga. Sizingatheke kuti zinthu zisayende mokomera moyo wanga. Sindingalephere; sindingadwale; sindingagonjetsedwe. Ndimasuntha kuchoka pa kupambana kupitanso pa kupambana kwina mu dzina la Yesu!

#ZitsimikizoZosalephera
#MoyoWosakanidwa

Pitanikuwebusaitiyathu: www.fountainofvictory.org

Komasotipezenipamasambaathuawa:
Facebook – https://www.facebook.com/fovchurchinternational

Facebook- https://www.facebook.com/pastorjosephziba

YouTube – https://www.youtube.com/channel/UCC4q8pRvbxfxCmZ3M5BpcRg

Instagram – https://www.instagram.com/fovupdate

Twitter – https://www.twitter.com/fovupdate

share

Editorial Team of the FOVCI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *